Nkhani yomwe yamveka kuti pali mpungwepungwe ndi chinyengo pakayendetsedwe ka ngongole yomwe boma linakhazikitsa, ya Youth Enterprise Development Fund (YEDF), yomwe cholinga chake ndikutukula achinyamata m’dziko lino powapatsa ngongole yoyambira mabizinesi osiyanasiyana, ndiyomvetsa chisoni kwambiri.
Poyamba, tidamva mtsogoleri wa dziko lino pomwe ankakhazikitsa ngongoleyi kuti omwe alandire ngongoleyi ndi achinyamata okhaokhawo omwe ndi a chipani chawo, chomwe ndicholamula boma, cha Democratic Progressive Party (DPP).
Kenako, tikumva kuti Mafumu akumauza achinyamata omwe akufuna kupindula nawo ndi ngongoleyi kuti aziwapatsa ndalama kuti awasayinire mapepala ofunsira ngongoleyi.
Pano, tikumva kuti nduna ya achinyamata ndi zamasewero, a Lucius Kanyumba, akumanka nayendayenda m’maboma a dziko lino kukumana ndi aphungu a kunyumba ya malamulo omwe ndi a DPP okhaokha, nkumawafotokozera momwe achinyamata a m’madera mwawo angapindule ndi ngongoleyi. Izi n’zokhumudwitsa kwambiri kwa wina aliyense amene amalifunira dziko lino zabwino.
Kwa nthawi yayitali achinyamata a m’dziko lino, omwe ndi atsogoleri amawa, akhala akulira kuti boma ndi makampani osiyanasiyana sakukhazikitsa mwayi woti achinyamata azipeza nchito akamaliza sukulu. Mwachitsanzo, boma ndi makampaniwa pamodzi ndi mabungwe omwe siaboma, amapempha kuti munthu amene akufuna kumulemba nchito akhale atagwirapo nchito yangati yomweyo kwa zaka zina zambiri. Izi zikupangitsa kuti achinyamata ambiri akhale paulova wa dzaoneni m’dziko lino chifukwa choti achinyamatawa amakhala kuti angochoka kusukulu kumene ndipo amakhala alibe mbiri yina yiri yonse yanchito. Pamapeto pake, achinyamata ambiri sakupeza mwayi wa nchito m’dziko lino. Izi n’zochita kuonekeratu.
Kotero, anthu ambiri m’dziko lino amaona kuti m’mene boma lakhazikitsa ngongole ya achinyamatayi, yithandiza achinyamata omwe ali paulova wadzaoneniyu kuti ayambe timabizinesi tosiyanasiyana ndi kumapeza zofuna zamoyo wawo watsikunditsiku.
Koma chokhumudwitsa n’chakuti pali anthu ena monga mafumu ena adyera ndi anthu andale makamaka achipani cholamula m’dziko lino cha DPP, akufuna kupondereza achinyamata ena kuti asakhale ndi mwayi olandila nawo ngongoleyi. Zachisoni ndithu.
Kodi mafumuwa popempha kuti achinyamatawa azipereka ndalama kwa iwowa akuona ngati achinyamatawa aziyipeza kuti ndalamayo? Kodi m’chitidweyu sichinyengo chomwe boma limaletsa m’dziko lino? Mesa iwowo mafumuwa ndi nchito yawo ndipo amalandira malipiro anchitoyi kuchokera kuboma? Ndiye chowapatsira kangachepe ndi chiyani? M’chitidwe onyasawu utha kupangitsa kuti achinyamata amene alibe ndalama yomwe mafumuwa amafuna, asalandile nawo ngongoleyi.
Zomwenso boma likuchita pomakumana ndi aphungu a DPP okhaokha kumawauza m’mene achinyanyamata am’madera mwawo angapezere mwayi olandila nawo ngongoleyi, zikuyenera kudzudzulidwa kwambiri.
Angangakhale izi sizikubwera ngati zodabwitsa, pokumbukira mawu omwe mtsogoleri wa dziko lino adanena tsiku limene ankakhazikitsa ngongoleyi, kuti achinyamata okhaokhawo omwe ndi otsatira awo ndiamene alandire ngongoleyi, tiyenera kukambapo kuti izi zikutsutsana ndi mfundo za demokalase zomwe chipani cha DPP chimalalika kuti ndingodya zake.
Chomwe boma liyenera kudziwa ndichakuti siachinyamata okhawo omwe ndi otsatira achipani cha DPP, amene ali paumphawi wadzaoneni.
Komanso, kukondera anthu achipani cholamula boma chokhachokha ndikosayenera chifukwa ngongoleyi ndi ya boma ndipo ndalama yake yinachokera kumsonkho omwe anthu amapereka m’dziko lino. Siotsatira chipani cha DPP okha omwe amapereka msonkho kuboma. Boma liyenera kugawa ngongoleyi mwachilungamo ndimosakondera kuti yipindulire achinyamata ovutikadi m’dziko lino. Komanso mafumu omwe akufuna kumadyera achinyamata ovutikawa pomawapempha ndalama ayenera kunjatidwa kuti aone polekera ndi m’chitidwe waumvewu.
No comments:
Post a Comment